LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w24 May masa. 20-25
  • Mmene Mungapezele Womanga Naye Banja

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mmene Mungapezele Womanga Naye Banja
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KUPEZA MUNTHU WOYENELELA
  • DEKHANI KUTI MUMUYANG’ANILE BWINO
  • KUYAMBA CIBWENZI
  • KODI ENA ANGAWATHANDIZE BWANJI AKHRISTU AMENE NI MBETA?
  • Mmene Mungakhalile pa Cibwenzi Copambana
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Khalani Okhulupilika kwa Wina ndi Mnzake
    N’zotheka Banja Lanu Kukhala Lacimwemwe
  • Cikwati Ni Mphatso Yocokela Kwa Mulungu
    Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu
  • Cikwati Ndi Mphatso Yocokela kwa Mulungu Wacikondi
    “Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu”
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
w24 May masa. 20-25

NKHANI YOPHUNZILA 21

NYIMBO 107 Cikondi ca Umulungu

Mmene Mungapezele Womanga Naye Banja

“Kodi ndi ndani amene angapeze mkazi wamakhalidwe abwino? Ndi wamtengo wapatali kuposa miyala ya kolali.”—MIY. 31:10.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Mfundo za m’Baibo zimene zingathandize munthu kupeza mnzake womuyenelela amene angamange naye banja. Komanso mmene mpingo ungathandizile amene akufuna kudzaloŵa m’banja.

1-2. (a) Kodi Akhristu amene ni mbeta ayenela kuganizila zinthu ziti asanayambe cibwenzi? (b) Kodi kukhala pa “cibwenzi” kutanthauza ciyani? (Onani “Kufotokozela Mawu Ena.”)

KODI mumafuna kudzaloŵa m’banja? Ngakhale kuti cimwemwe ceniceni sicidalila kuloŵa m’banja, Akhristu ambili amene ni mbeta, acinyamata ngakhale akulu-akulu omwe, amayembekezela mwacidwi kupeza munthu wodzamanga naye banja. Komabe, musanayambe cibwenzi, muyenela kukhala wokonzeka kuloŵa m’banja kuthupi, kuuzimu, komanso m’maganizo.a (1 Akor. 7:36) Kucita zimenezi kudzakuthandizani kuti mudzakhale na banja lacimwemwe.

2 Komabe, si nthawi zonse pamene cimakhala capafupi kupeza munthu womanga naye banja. (Miy. 31:10) Ndipo ngakhale mutapeza munthu amene mufuna kum’dziŵa bwino, kungakhale kovutabe kuyamba cibwenzi.b M’nkhani ino, tikambilane zimene zingathandize Akhristu amene ni mbeta kupeza munthu woyenelela na kuyamba cibwenzi. Tikambilanenso mmene ena mu mpingo angathandizile amene akufuna kudzaloŵa m’banja.

KUPEZA MUNTHU WOYENELELA

3. Kodi Mkhristu amene ni mbeta ayenela kuganizila ciyani pofuna-funa munthu womanga naye banja?

3 Ngati mufuna kudzaloŵa m’banja, ni bwino kudziŵilatu makhalidwe amene mukufuna mwa munthu wodzamanga naye banja. Mukapanda kutelo, mungaphonye munthu wokuyenelelani, kapena mungayambe cibwenzi na munthu wosakuyenelelani. Munthu wokuyenelelani, ni Mkhristu wobatizika. (1 Akor. 7:39) Koma izi sizitanthauza kuti Mkhristu aliyense wobatizika angakhale wokuyenelelani. Conco, dzifunseni kuti: ‘Kodi nili na zolinga zotani pa umoyo wanga? Ni makhalidwe ati amene nifuna mwa munthu amene ningakonde kudzamanga naye banja? Kodi zimene nikufunazo mwa munthu winayo ni zotheka?’

4. Ni zinthu ziti zimene ena amachula m’mapemphelo awo?

4 Ngati mufuna kudzaloŵa m’banja, n’zosacita kufunsa kuti mumaipemphelela nkhaniyi kuti mukapeze munthu wokuyenelelani. (Afil. 4:6) Zoona zake n’zakuti, Yehova salonjeza kuti adzasankhila aliyense munthu wodzakwatilana naye. Ngakhale n’telo, iye amasamala zofuna zanu komanso mmene mukumvela, ndipo adzakuthandizani pamene mufuna-funa munthu wokuyenelelani. Conco, pitilizani kumuuza zofuna zanu komanso mmene mukumvela. (Sal. 62:8) Pemphelani kuti akupatseni nzelu, komanso kuti mukhale woleza mtima. (Yak. 1:5) M’bale Johnc wa ku America amene ni mbeta anafotokoza zimene amachula m’mapemphelo ake. Iye anati: “Nimauza Yehova makhalidwe amene nifuna mwa munthu amene ningakonde kudzamanga naye banja. Nimapemphela kuti nikhale na mipata yokumana na munthu woniyenelela. Nimapemphanso Yehova kuti anithandize kukulitsa makhalidwe amene anganithandize kudzakhala mwamuna wabwino nikadzakwatila.” Tanya, mlongo wa ku Sri Lanka amene ni mbeta, anati: “Pamene nikufuna-funa munthu woniyenelela, nimapempha Yehova kuti anithandize kukhala wokhulupilika, wa maganizo abwino, komanso wacimwemwe.” Ngakhale kuti simunapeze munthu wokuyenelelani nthawi yomweyo, Yehova analonjeza kuti adzakusamalilani kuthupi, na kukuonetsani cikondi cimene mufunikila.—Sal. 55:22.

5. Pali mipata yanji imene mbeta ingapezele munthu wokonda Yehova? (1 Akorinto 15:58) (Onaninso cithunzi.)

5 Baibo imatilimbikitsa kuti tizikhala na “zocita zambili pa nchito ya Ambuye.” (Ŵelengani 1 Akorinto 15:58.) Conco, pitilizani kukhala na zocita zambili mu utumiki wa Yehova na kukhala na maceza pamodzi na abale na alongo osiyana-siyana. Mukatelo, mudzakhala na maceza olimbikitsa, komanso mwayi wokumana na Akhristu ena amene ni mbeta, amene nawonso amaika maganizo awo pa kutumikila Yehova. Ndipo pamene mucita zonse zotheka kuti mukondweletse Yehova, mudzapeza cimwemwe ceniceni.

Zithunzi: 1. Mlongo amene ni mbeta akuceza mwacimwemwe na mlongo wacikulile pamene ali mu ulaliki. 2. Mlongoyo akugaŵila ena cakudya pomwe ali pa nchito yamamangidwe a gulu. 3. M’bale amene ni mbeta wapita na mkulu kukacita ulendo waubusa ku banja lina lake. 4. M’baleyo akuseŵenzetsa makina odulila zinthu pa nchito yamamangidwe imodzimodziyo.

Mukamakhala na zocita zoculuka mu utumiki wa Yehova, na kuceza na abale na alongo osiyana-siyana, mungakumane na ena amene nawonso akufuna kuloŵa m’banja (Onani ndime 5)


6. Kodi Akhristu amene akufuna-funa munthu womanga naye banja ayenela kukumbukila ciyani?

6 Koma pali cenjezo: Nkhani yofuna munthu womanga naye banja isamacite kutengelatu maganizo anu onse. (Afil. 1:10) Cimwemwe ceniceni sicidalila kukhala mbeta kapena kukhala pabanja, cimadalila ubale wanu na Yehova. (Mat. 5:3) Ndipo pamene mukali mbeta, muli na mipata yoculuka yowonjezela utumiki wanu (1 Akor. 7:​32, 33) Seŵenzetsani nthawi yanu ya umbeta mwanzelu. Jessica, mlongo wa ku America amene anakwatiwa atayandikila zaka 40 anati, “N’nali wokangalika mu utumiki, ndipo izi zinanithandiza kukhala wokhutila ngakhale kuti n’nali wofunitsitsa kukwatiwa.”

DEKHANI KUTI MUMUYANG’ANILE BWINO

7. N’cifukwa ciyani n’kwanzelu kuyamba mwamuyang’anila munthu capatali musanamufunsile? (Miyambo 19:2)

7 Bwanji ngati mwaona munthu amene muganiza kuti angakhale wokuyenelelani? Kodi muyenela kumufikila nthawi yomweyo? Baibo imakamba kuti munthu wocenjela amafufuza asanacitepo kanthu. (Ŵelengani Miyambo 19:2.) Conco, n’kwanzelu kuyamba mwamuyang’anila capatali musanamuuze maganizo anu. M’bale Aschwin wa ku Netherlands ananena kuti: “Cikondi cikhoza kuyaka mwamsanga, komanso kuzima mwamsanga. Conco, m’malo moyamba cibwenzi mopupuluma, tengankoni nthawi kuti mumuyang’anile bwino munthuyo.” N’kutheka kuti pomuyang’anila munthuyo, mungapeze kuti iye si wokuyenelelani.

8. Kodi kuyang’anila munthu capatali kuyenela kucitika motani? (Onaninso cithunzi.)

8 Kodi kuyang’anila munthu capatali kuyenela kucitika motani? Pa misonkhano ya mpingo kapena pa maceza a gulu, mungadziŵeko zinthu zina zokhudza munthuyo monga uzimu wake, umunthu wake, komanso makhalidwe ake. Kodi ali na mabwenzi otani, ndipo amakonda kukamba zinthu zotani? (Luka 6:45) Kodi zolinga zake n’zofanana ni zanu? Mungafunseko akulu a mu mpingo mwawo, kapena Akhristu okhwima amene amam’dziŵa bwino. (Miy. 20:18) Mungawafunse za mbili yake, komanso makhalidwe ake. (Rute 2:11) Pamene mukuyang’anila munthuyo capatali, samalani kuti musamukhumudwitse na kacitidwe kanu. Musungileni ulemu wake, pewani kumulondalonda, kapena kuloŵelela m’nkhani za munthu mwini.

Zithunzi: M’bale na mlongo amene taonetsa aja, akuyang’anilana capatali pa misonkhano ya mpingo. 1. Mlongoyo akuyang’ana mmene m’baleyo akucitila zinthu na banja lacikulile. 2. M’bale akuyang’ana mmene mlongoyo akukwanilitsila mbali ya ophunzila pa msonkhano wa mkati mwa mlungu.

Musanafikile munthu kuti muyambe naye cibwenzi, muyang’anileni kwa kanthawi (Onani ndime 7-8)


9. Musanamufunsile munthu, kodi muyenela kukhala wotsimikiza za ciyani?

9 Kodi muyenela kumuyang’anila kwa utali wanji kuti mumufikile? Mukamufikila mofulumila angakuoneni kuti ndinu wopupuluma. (Miy. 29:20) Koma ngati mungatenge nthawi yaitali kwambili, angakuoneni kukhala munthu wokayika-kayika, wosadziŵa bwino cimene afuna, maka-maka akazindikila kuti mumamufuna. (Mlal. 11:4) Komanso kumbukilani kuti, musanamufikile munthuyo musakhale wotsimikiza na mtima wonse kuti mudzakwatilana naye basi. M’malo mwake, khalani wotsimikiza kuti inuyo ndinu wokonzeka kuloŵa m’banja, komanso kuti n’kutheka munthu winayo angakhale mnzanu wokuyenelelani.

10. Muyenela kucita bwanji mukaona kuti munthu wina akukufunani, koma inu simumufuna?

10 Koma bwanji ngati mwaona kuti munthu wina akukufunani? Ngati inuyo simukumufuna, onetsani zimenezo mwa kacitidwe kanu. Kungakhale kupanda cikondi kucita zinthu moonetsa ngati inunso mukufuna kukhala naye pa cibwenzi, pamene sizili conco.—1 Akor. 10:24; Aef. 4:25.

11. Kodi amene amakhala na udindo wopezela munthu cibwenzi kapena womanga naye banja, ayenela kukumbukila mfundo ziti?

11 Ku maiko ena, makolo kapena acibale ena acikulile ni amene amasankhila munthu womanga naye banja. Koma kwina, acibale kapena mabwenzi amangokupezela munthu amene ungayambe naye cibwenzi. Iwo amalinganiza zakuti mukakumane kuti muone ngati ndinu oyenelelana. Mukapemphedwa kuti mupezele wina cibwenzi, kapena womanga naye banja, muziganizila zimene aliyense wa iwo akufuna. Mukapeza munthu amene muona kuti angakhale woyenelela, fufuzani zambili zokhudza umunthu wake na makhalidwe ake, koma maka-maka uzimu wake. Kukhala pa ubale wolimba na Yehova kumaposa ndalama, maphunzilo, ngakhale kuchuka. Komabe, kumbukilani kuti aŵiliwo ndiwo ayenela kupanga cisankho, kaya kukwatilana kapena ayi.—Agal. 6:5.

KUYAMBA CIBWENZI

12. Ngati mufuna kukhala pa cibwenzi na munthu wina wake, kodi mungamufikile motani?

12 Mukafuna kuyamba cibwenzi na wina wake, kodi mungamufikile bwanji?d Mungam’pemphe kuti mukambilane na munthuyo pamaso-m’pamaso kapena pa foni. Muuzeni maganizo anu momveka bwino. (1 Akor. 14:9) Mungafunikile kum’patsa mpata kuti aganizilepo. (Miy. 15:28) Ndipo ngati munthuyo safuna, musamukakamize.

13. Kodi muyenela kucita bwanji munthu wina akakufunsilani? (Akolose 4:6)

13 Nanga bwanji ngati munthu wina wakufunsilani? Dziŵani kuti munthuyo wacita kulimba mtima kuti akufikileni. Conco, citani naye mokoma mtima, komanso mwaulemu. (Ŵelengani Akolose 4:6.) Ngati mufuna nthawi kuti muganizilepo, muuzeni zimenezo. Komabe, pasapite nthawi yaitali musanapeleke yankho. (Miy. 13:12) Ngati simunamukonde munthuyo, mufotokozeleni zimenezo mokoma mtima, komanso momveka bwino. Onani mmene m’bale Hans wa ku Austria anacitila pamene mlongo anamufikila. Iye anati: “N’namuuza maganizo anga mokoma mtima, komanso momveka bwino. N’namuuza mwamsanga cifukwa sin’nafune kum’patsa ciyembekezo cabodza. Pa cifukwa cimeneci, n’nayamba kucita naye zinthu mosamala.” Koma ngati inunso mufuna kukhala naye pa cibwenzi, muuzeni maganizo anu, komanso zimene mukuyembekezela pa cibwenzi canu. Zimene mufuna zingakhale zosiyana na zimene mnzanuyo akuyembekezela malinga na cikhalidwe ca kwanu, komanso zinthu zina.

KODI ENA ANGAWATHANDIZE BWANJI AKHRISTU AMENE NI MBETA?

14. Kodi tingawalimbikitse bwanji Akhristu amene ni mbeta na mawu athu?

14 Kodi tonsefe tingawathandize bwanji Akhristu amene akufuna kuloŵa m’banja? Njila imodzi ni kusamala zimene timakamba. (Aef. 4:29) Tingadzifunse kuti: ‘Kodi nimakamba mawu acipongwe kwa anthu amene afuna kuloŵa m’banja? Nikaona m’bale wosakwatila na mlongo wosakwatiwa akukambitsana, kodi nimaganiza kuti akufunana?’ (1 Tim. 5:13) Kuwonjezela apo, tisamapangitse Akhristu amene ni mbeta kuona kuti ali na vuto linalake kapena akumanidwa zina zake cifukwa sali pa banja. M’bale Hans amene tam’chula uja anakamba kuti: “Abale ena amanifunsa kuti, ‘N’cifukwa ciyani sukukwatila? Wakula tsopano.’ Mawu ngati amenewa amapangitsa Akhristu amene sali pa banja kuona kuti sayamikilidwa, ndipo zingawapangitse kuyamba kuganizila kwambili zoloŵa m’banja.” M’malo monena mawu ngati amenewa, zingakhale bwino kwambili kupeza mipata yoyamikila Akhristu amene ni mbeta.—1 Ates. 5:11.

15. (a) Malinga na mfundo ya pa Aroma 15:​2, kodi tiyenela kuganizila ciyani tisanathandize munthu kupeza woloŵa naye m’banja? (Onaninso cithunzi.) (b) Ni mfundo zolimbikitsa ziti zimene munapeza mu vidiyo?

15 Nanga bwanji ngati tiona kuti m’bale na mlongo wina wake angayenelelane? Baibo imatiuza kuti tiyenela kuganizila zofuna za ena. (Ŵelengani Aroma 15:2.) Akhristu ambili amene ni mbeta, safuna zowapezela mwamuna kapena mkazi. Ndipo tiyenela kulemekeza maganizo awo. (2 Ates. 3:11) Ena angayamikile kuwathandiza, koma sitiyenela kucita zimenezo ngati sanatipemphe.e (Miy. 3:27) Ena amafuna thandizo, koma osati lacindunji. Mwa citsanzo, Lydia mlongo wa ku Germany amene ni mbeta anati: “Mungaitane m’bale na mlongoyo pa maceza a anthu ambili. Kungopeleka mpata kuti aŵiliwo aonane, kenaka n’kusiya zonse m’manja mwawo.”

Mlongo uja na m’bale mmodzimodziyo, akuceza pomwe ali pa maceza a gulu.

Kukhala pa gulu kumapeleka mpata kwa Akhristu amene ni mbeta kuti akumane (Onani ndime 15)


16. Kodi Akhristu amene ni mbeta ayenela kukumbukila ciyani?

16 Tonsefe—kaya ndife mbeta kapena tili pa banja—tingakhale na moyo wacimwemwe komanso wokhutilitsa! (Sal. 128:1) Conco, ngati mufuna kuloŵa m’banja koma musanapeze munthu wokuyenelelani, pitilizani kuika maganizo anu pa utumiki wanu kwa Yehova. Mlongo Sin Yi wa ku Macao ananena kuti: “Nthawi imene tingakhale mbeta ni yaifupi kwambili poyelekezela na nthawi imene tidzakhale na mnzathu wa mu ukwati m’Paradaiso. Sangalalani na nthawiyo, ndipo iseŵenzetseni mwanzelu.” Nanga bwanji ngati munapeza munthu amene muona kuti ni wokuyenelelani, ndipo munayamba naye cibwenzi? M’nkhani yotsatila tidzakambilana mmene mungakhalile na cibwenzi copambana.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Muyenela kutani kuti mupeze munthu woloŵa naye m’banja?

  • N’cifukwa ciyani n’kwanzelu kuyamba mwamuyang’anila capatali munthu amene mufuna kuyamba naye cibwenzi?

  • Kodi ena mu mpingo angawathandize bwanji Akhristu amene afuna kuloŵa m’banja?

NYIMBO 137 Azimayi Okhulupilika, Alongo Athu

a Kuti mudziŵe ngati ndinu wokonzeka kuloŵa m’banja, onani nkhani yakuti, “Kukhala Pacibwenzi—Mbali Yoyamba: Kodi Ndine Wokonzeka Kukhala Pacibwenzi?” pa jw.org ku Chichewa.

b KUFOTOKOZELA MAWU ENA: M’nkhani ino komanso yotsatila, mawu akuti “cibwenzi” atanthauza nthawi pamene mwamuna na mkazi amafuna kudziŵana bwino kuti aone ngati ni oyenelelana kukamanga banja. Cibwenzi cimayamba pa nthawi imene aŵiliwo agwilizana kutelo, mpaka pamene adzagwilizane kucithetsa, kapena kutomelana kuti akakwatilane.

c Maina ena asinthidwa.

d M’zikhalidwe zina, kambili m’bale ndiye amafunsila mlongo. Komabe, sikulakwa mlongo kufikila m’bale. (Rute 3:​1-13) Kuti mudziŵe zambili pa nkhaniyi, onani nkhani yakuti, “Acinyamata Akufunsa Kuti . . . Kodi Mnyamata Ndingamuuze Bwanji Kuti Ndikumufuna?” mu Galamukani! ya November 8, 2004.

e Onani vidiyo yakuti Omenya Nkhondo ya Cikhulupililo Mwacipambano—Akhristu Amene Sali Pabanja pa jw.org.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani