Tsiku Laciŵili
“Adzakupezeni opanda banga, opanda cilema ndiponso muli mu mtendele”—2 Petulo 3:14
M’maŵa
8:20 Vidiyo ya Nyimbo
8:30 Nyimbo Na. 58 na Pemphelo
8:40 YOSIYILANA: Muzikhala Okonzeka Kuuzako Ena “Uthenga Wabwino wa Mtendele”
• Musaleke Kukhala Okangalika (Aroma 1:14, 15)
• Muzikonzekela Bwino (2 Timoteyo 2:15)
• Muziyambitsa Ndinu Makambilano (Yohane 4:6, 7, 9, 25, 26)
• Kasonkhezeleni Cidwi Cisanazizile (1 Akorinto 3:6)
• Thandizani Ophunzila Baibo Kukhwima Kuuzimu (Aheberi 6:1)
9:40 Inu Acinyamata—Sankhani Njila Yobweletsa Mtendele! (Mateyu 6:33; Luka 7:35; Yakobo 1:4)
10:00 Nyimbo Na. 135 na Zilengezo
10:10 VIDIYO: Mmene Abale Akukhalilabe pa Mtendele Olo Kuti Akukumana na . . .
• Otsutsa
• Matenda
• Mavuto a Zacuma
• Ngozi Zacilengedwe
10:45 UBATIZO: Pitilizani Kuyenda “Panjila Yamtendele” (Luka 1:79; 2 Akorinto 4:16-18; 13:11)
11:15 Nyimbo Na. 54 na Kupumula
masana
12:35 Vidiyo ya Nyimbo
12:45 Nyimbo Na. 29
12:50 YOSIYILANA: Pewani Zinthu Zosokoneza Mtendele
• Kudzitama (Aefeso 4:22; 1 Akorinto 4:7)
• Kaduka (Afilipi 2:3, 4)
• Kusaona Mtima (Aefeso 4:25)
• Mijedo Yovulaza (Miyambo 15:28)
• Mkwiyo Wosadziletsa (Yakobo 1:19)
13:45 SEŴELO LA M’BAIBO: Yehova Akutitsogolela Panjila ya Mtendele—Gawo 1 (Yesaya 48:17, 18)
14:15 Nyimbo Na. 130 na Zilengezo
14:25 YOSIYILANA: ‘Pezani Mtendele ndi Kuusunga’ . . .
• Mwa Kupewa Mtima wa Pacala (Miyambo 19:11; Mlaliki 7:9; 1 Petulo 3:11)
• Mwa Kupepesa (Mateyu 5:23, 24; Machitidwe 23:3-5)
• Mwa Kukhululuka na Mtima Wonse (Akolose 3:13)
• Mwa Kuseŵenzetsa Mwanzelu Mphatso ya Kulankhula (Miyambo 12:18; 18:21)
15:15 Yesetsani Kusunga “Umodzi Wathu . . . Mwamtendele”! (Aefeso 4:1-6)
15:50 Nyimbo Na. 113 na Pemphelo Lothela