CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | MATEYU 4-5
Zimene Tiphunzilapo pa Ulaliki wa Yesu wa pa Phili
Kodi mumazindikila zosoŵa zanu zauzimu?
Mau akuti “anthu amene amazindikila zosoŵa zawo zauzimu,” atanthauza anthu opempha-pempha mzimu wa Mulungu. (Mat. 5:3.) Tingaonetse kuti ndise ofunitsitsa kulandila thandizo lauzimu locokela kwa Mulungu mwa. . .
kuŵelenga Baibo tsiku lililonse
kumakonzekela misonkhano na kupezekapo
kuŵelenga zofalitsa zathu, ndipo ngati n’zotheka, kumaŵelenganso nkhani zina zopezeka pa webusaiti yathu
kumatamba pulogilamu ya JW Broadcasting ya mwezi uliwonse
Ningakulitse bwanji cizoloŵezi ca kumadya cakudya cauzimu?