CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | 2 PETULO 1-3
‘Muzikumbukira Kukhalapo kwa Tsiku la Yehova’
Yehova adzabweretsa chiweruzo pa nthawi imene anakonza. Kodi zochita zathu zimasonyeza kuti takonzekera kubwera kwa tsiku limeneli?
Kodi ‘kukhala anthu akhalidwe loyera ndiponso kuchita ntchito zosonyeza kuti ndinu odzipereka kwa Mulungu’ kumatanthauza chiyani?
Kumatanthauza kutsatira mfundo za Yehova pa nkhani ya mmene tiyenera kuonera zinthu zabwino kapena zoipa komanso kusagonja ena akamatsutsa zimene timakhulupirira
Kumatanthauza kuyesetsa nthawi zonse kuchita zinthu zokhudza kulambira kwathu, tikakhala kwatokha kapena pagulu