NYIMBO 87
Bwerani Mudzasangalale
zosindikizidwa
1. Tikukhala m’dziko lomwe n’loipa;
Anthu sakudziwa M’lungu.
Choncho tifunikatu malangizo,
Oti atitsogolere.
Misonkhano yathu imathandiza;
Kukhala osangalala.
Timamvako mawu olimbikitsa
Cholinga tisafooke.
Sitidzasiya kugwiritsa ntchito;
Malamulo a Yehova.
Pamisonkhano timalangizidwa;
Kukondatu choonadi.
2. Yehova amadziwa bwino zinthu;
Zomwe tikufunikira.
Tikamasonkhana timasonyeza
Kuti timamudalira.
Malangizo ochoka kwa akulu,
Amatithandiza zedi.
Timadziwa kuti sitili tokha,
Iwo adzatithandiza.
Choncho poyembekezera m’tsogolo,
Tisasiye kusonkhana.
Tiziphunzira kugwiritsa ntchito
Nzeru yochoka kumwamba.
(Onaninso Sal. 37:18; 140:1; Miy. 18:1; Aef. 5:16; Yak. 3:17.)