Genesis
5 Tsopano nayi mbiri ya Adamu. M’tsiku limene Mulungu analenga Adamu, anam’panga iye m’chifaniziro cha Mulungu.+ 2 Anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi.+ Kenako, anawadalitsa ndi kuwatchula dzina lakuti Anthu,+ m’tsiku limene anawalenga.+
3 Adamu atakhala ndi moyo zaka 130, anabereka mwana wamwamuna m’chifaniziro chake, wofanana naye. Anamutcha dzina lake Seti.+ 4 Adamu atabereka Seti, anakhalabe ndi moyo zaka zina 800. Pa zaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.+ 5 Chotero, masiku onse amene Adamu anakhala ndi moyo anakwana zaka 930, kenako anamwalira.+
6 Seti atakhala ndi moyo zaka 105, anabereka Enosi.+ 7 Atabereka Enosi, Seti anakhalabe ndi moyo zaka zina 807. Pa zaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 8 Chotero, masiku onse a Seti anakwana zaka 912, kenako anamwalira.
9 Enosi atakhala ndi moyo zaka 90, anabereka Kenani.+ 10 Atabereka Kenani, Enosi anakhalabe ndi moyo zaka zina 815. Pa zaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 11 Chotero, masiku onse a Enosi anakwana zaka 905, kenako anamwalira.
12 Kenani atakhala ndi moyo zaka 70, anabereka Mahalalele.+ 13 Atabereka Mahalalele, Kenani anakhalabe ndi moyo zaka zina 840. Pa zaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 14 Chotero, masiku onse a Kenani anakwana zaka 910, kenako anamwalira.
15 Mahalalele atakhala ndi moyo zaka 65, anabereka Yaredi.+ 16 Atabereka Yaredi, Mahalalele anakhalabe ndi moyo zaka zina 830. Pa zaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 17 Chotero, masiku onse a Mahalalele anakwana zaka 895, kenako anamwalira.
18 Yaredi atakhala ndi moyo zaka 162, anabereka Inoki.+ 19 Atabereka Inoki, Yaredi anakhalabe ndi moyo zaka zina 800. Pazaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 20 Chotero, masiku onse a Yaredi anakwana zaka 962, kenako anamwalira.
21 Inoki atakhala ndi moyo zaka 65, anabereka Metusela.+ 22 Atabereka Metusela, Inoki anayendabe ndi Mulungu woona kwa zaka 300. Pa zaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 23 Chotero, masiku onse a Inoki anakwana zaka 365. 24 Inoki anayendabe+ ndi Mulungu woona.+ Kenako iye sanaonekenso, chifukwa Mulungu anam’tenga.+
25 Metusela atakhala ndi moyo zaka 187, anabereka Lameki.+ 26 Atabereka Lameki, Metusela anakhalabe ndi moyo zaka zina 782. Pa zaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 27 Chotero, masiku onse a Metusela anakwana zaka 969, kenako anamwalira.
28 Lameki atakhala ndi moyo zaka 182, anabereka mwana wamwamuna. 29 Mwanayo anamutcha dzina lakuti Nowa,+ ndipo anati: “Uyu ndi amene adzatibweretsere mpumulo ku ntchito yathu yopweteketsa manja, chifukwa cholima nthaka imene Yehova anaitemberera.”+ 30 Atabereka Nowa, Lameki anakhalabe ndi moyo zaka zina 595. Pa zaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 31 Chotero masiku onse a Lameki anakwana zaka 777, kenako anamwalira.
32 Nowa anakwanitsa zaka 500. Pambuyo pake iye anabereka Semu,+ Hamu+ ndi Yafeti.+