Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide. Nyimbo ya chikumbutso.+
70 Inu Mulungu, fulumirani kundilanditsa,+
Inu Yehova, fulumirani kundithandiza.+
2 Amene akufunafuna moyo wanga achite manyazi ndi kuthedwa nzeru.+
Amene akukondwera ndi tsoka langa abwerere ndipo anyazitsidwe.+
3 Amene akunena kuti: “Eyaa! Eyaa!” abwerere chifukwa cha manyazi awo.+
4 Onse amene akufunafuna inu akondwere ndi kusangalala mwa inu,+
Ndipo onse amene amakonda chipulumutso chanu, nthawi zonse azinena kuti: “Mulungu alemekezeke!”+
5 Koma ine ndasautsika ndipo ndasauka.+
Inu Mulungu, chitanipo kanthu mwamsanga kuti zinthu zindiyendere bwino.+
Inu ndinu thandizo langa ndi Wopereka chipulumutso kwa ine.+
Inu Yehova musachedwe.+