3 Akabisala pamwamba pa phiri la Karimeli, ndidzawafufuza mosamala ndi kuwatenga,+ ndipo akathawa pamaso panga ndi kubisala pansi pa nyanja,+ ndidzalamula njoka pansi pa nyanja pomwepo kuti iwalume.
18 M’chikondi mulibe mantha,+ koma chikondi chimene chili chokwanira chimathetsa mantha,+ chifukwa mantha amachititsa munthu kukhala womangika. Amene ali ndi mantha, chikondi chake si chokwanira.+