6 Iye ananenanso kuti: “Ndine Mulungu wa atate ako, Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo.”+ Pamenepo Mose anaphimba nkhope yake, chifukwa anaopa kuyang’ana Mulungu woona.
32 ‘Ine ndine Mulungu wa makolo ako. Ndine Mulungu wa Abulahamu, wa Isaki ndi wa Yakobo.’+ Ponjenjemera ndi mantha, Mose sanathenso kupitiriza kuyang’anitsitsa chitsambacho.