6 Iye ananenanso kuti: “Ndine Mulungu wa atate ako, Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo.”+ Pamenepo Mose anaphimba nkhope yake, chifukwa anaopa kuyang’ana Mulungu woona.
26 Koma zakuti akufa amaukitsidwa, kodi inu simunawerenge m’buku la Mose, m’nkhani ya chitsamba chaminga, mmene Mulungu anamuuzira kuti, ‘Ine ndine Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo’?+
37 Koma zakuti akufa amaukitsidwa ngakhalenso Mose anafotokoza m’nkhani ya chitsamba cha minga.+ M’nkhani imeneyo iye ananena kuti Yehova ndi ‘Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo.’+