Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 35:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Isiraeli atamanga msasa+ m’dziko limenelo, Rubeni anagona ndi Biliha mkazi wamng’ono* wa bambo ake, ndipo Isiraeli anamva zimene zinachitikazo.+

      Yakobo anali ndi ana aamuna 12.

  • Genesis 37:22
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 22 Ndipo anapitiriza kuwauza kuti: “Musakhetse magazi ayi.+ Muponyeni m’chitsime chopanda madzichi kutchire kuno, musamuvulaze.”+ Cholinga chake chinali chakuti amupulumutse kwa iwo ndi kum’bwezera kwa bambo ake.

  • Genesis 49:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 “Rubeni, iwe ndiwe mwana wanga woyamba kubadwa,+ nyonga yanga ndi poyambira mphamvu zanga zobereka.+ Unayenera kukhala ndi ulemu wopambana ndi mphamvu zopambana.

  • Ekisodo 6:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Tsopano awa ndiwo atsogoleri a nyumba ya makolo a Aisiraeli. Ana aamuna a Rubeni, yemwe anali mwana woyamba kubadwa wa Isiraeli,+ anali Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karami.+ Amenewa ndiwo mabanja a fuko la Rubeni.+

  • 1 Mbiri 5:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Mwana woyamba wa Isiraeli anali Rubeni.+ Iye anali woyamba kubadwa+ koma chifukwa chakuti anaipitsa bedi la bambo wake,+ udindo wake monga woyamba kubadwa unaperekedwa kwa ana a Yosefe,+ mwana wa Isiraeli. Choncho iye sanalembedwe monga woyamba kubadwa pamndandanda wa mayina wotsatira makolo.

  • Chivumbulutso 7:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Mu fuko la Yuda,+ anadindamo anthu 12,000.

      Mu fuko la Rubeni,+ 12,000.

      Mu fuko la Gadi,+ 12,000.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena