14 Tsopano awa ndiwo atsogoleri a nyumba ya makolo a Aisiraeli. Ana aamuna a Rubeni, yemwe anali mwana woyamba kubadwa wa Isiraeli,+ anali Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karami.+ Amenewa ndiwo mabanja a fuko la Rubeni.+
5Mwana woyamba wa Isiraeli anali Rubeni.+ Iye anali woyamba kubadwa+ koma chifukwa chakuti anaipitsa bedi la bambo wake,+ udindo wake monga woyamba kubadwa unaperekedwa kwa ana a Yosefe,+ mwana wa Isiraeli. Choncho iye sanalembedwe monga woyamba kubadwa pamndandanda wa mayina wotsatira makolo.