35 kuti magazi onse olungama okhetsedwa padziko lapansi abwere pa inu,+ kuyambira magazi a Abele+ wolungama+ mpaka magazi a Zekariya mwana wa Barakiya, amene inu munamupha pakati pa nyumba yopatulika ndi guwa lansembe.+
12 osati ngati Kaini, amene anachokera kwa woipayo n’kupha+ m’bale wake. N’chifukwa chiyani iye anapha m’bale wake? Chifukwa chakuti zochita zake zinali zoipa,+ koma za m’bale wake zinali zolungama.+