Numeri 22:32 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 32 Ndiyeno mngelo wa Yehova uja anam’funsa kuti: “N’chifukwa chiyani wakhala ukukwapula bulu wako maulendo atatu onsewa? Inetu ndabwera kudzakutchingira njira, chifukwa uli pa ulendo wothamangira kukachita zotsutsana ndi chifuniro changa.+ Deuteronomo 23:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Yehova Mulungu wanu sanafune kumvera Balamu,+ m’malomwake Yehova Mulungu wanu anakusinthirani temberero kukhala dalitso,+ chifukwa Yehova Mulungu wanu anakukondani.+ 2 Petulo 2:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Popeza anasiya njira yowongoka, asocheretsedwa. Atsatira njira ya Balamu+ mwana wa Beori, amene anakonda mphoto ya kuchita zoipa,+ Chivumbulutso 2:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 “‘Koma ngakhale zili choncho, ndakupeza ndi milandu ingapo. Iwe kumeneko uli ndi anthu olimbikira chiphunzitso cha Balamu,+ amene anaphunzitsa Balaki+ kuikira ana a Isiraeli chopunthwitsa kuti adye zoperekedwa nsembe kwa mafano ndi kuchita dama.+
32 Ndiyeno mngelo wa Yehova uja anam’funsa kuti: “N’chifukwa chiyani wakhala ukukwapula bulu wako maulendo atatu onsewa? Inetu ndabwera kudzakutchingira njira, chifukwa uli pa ulendo wothamangira kukachita zotsutsana ndi chifuniro changa.+
5 Yehova Mulungu wanu sanafune kumvera Balamu,+ m’malomwake Yehova Mulungu wanu anakusinthirani temberero kukhala dalitso,+ chifukwa Yehova Mulungu wanu anakukondani.+
15 Popeza anasiya njira yowongoka, asocheretsedwa. Atsatira njira ya Balamu+ mwana wa Beori, amene anakonda mphoto ya kuchita zoipa,+
14 “‘Koma ngakhale zili choncho, ndakupeza ndi milandu ingapo. Iwe kumeneko uli ndi anthu olimbikira chiphunzitso cha Balamu,+ amene anaphunzitsa Balaki+ kuikira ana a Isiraeli chopunthwitsa kuti adye zoperekedwa nsembe kwa mafano ndi kuchita dama.+