21 Kenako iwo anayamba kulankhulana kuti: “Ndithudi, izi zikuchitika chifukwa cha zimene tinachitira m’bale wathu uja.+ Pajatu tinaona kusautsika kwake pamene anatichonderera kuti timumvere chisoni, koma ife sitinalabadire. N’chifukwa chake tsokali latigwera.”+