26Tsopano m’dzikomo munagwanso njala, kuwonjezera pa njala yoyamba ija imene inagwa m’masiku a Abulahamu.+ Choncho Isaki anapita kwa Abimeleki, mfumu ya Afilisiti, ku Gerari.+
17 Farao atalola kuti ana a Isiraeli apite, Mulungu sanawadutsitse m’dziko la Afilisiti ngakhale kuti kunali kufupi, pakuti Mulungu anati: “Anthu angataye mtima atakumana ndi nkhondo ndipo angabwerere ku Iguputo.”+