Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 14:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Choncho iwo anafunsa Mose kuti: “Kodi watibweretsa kuno kuti tidzafere m’chipululu muno chifukwa chakuti mu Iguputo mulibe manda?+ N’chifukwa chiyani watichitira zimenezi, kutitulutsa mu Iguputo?

  • Ekisodo 16:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Ndipo ana a Isiraeli anali kunena kwa Mose ndi Aroni kuti: “Zikanakhala bwino dzanja la Yehova likanatiphera+ m’dziko la Iguputo, kumene tinali kudya nyama+ ndipo tinali kudya mkate ndi kukhuta. M’malomwake mwatibweretsa m’chipululu muno kuti muphetse mpingo wonsewu ndi njala.”+

  • Numeri 14:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 N’chifukwa chiyani Yehova watibweretsa kudziko lino kuti tidzaphedwe ndi lupanga?+ Akazi athu ndi ana athu adzatengedwa ndi adani.+ Kodi si bwino kuti tingobwerera ku Iguputo?”+

  • Nehemiya 9:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Choncho iwo anakana kumvera+ ndipo sanakumbukire+ zochita zanu zodabwitsa zimene munawachitira, m’malomwake anaumitsa khosi lawo+ ndipo anasankha mtsogoleri+ kuti awatsogolere pobwerera ku ukapolo wawo ku Iguputo. Koma inu ndinu Mulungu wokhululuka,+ wachisomo+ ndi wachifundo,+ wosakwiya msanga+ ndiponso wosonyeza kukoma mtima kosatha,+ chotero simunawasiye.+

  • Machitidwe 7:39
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 39 Koma makolo athu akale anakana kumumvera. M’malomwake, anamukankhira kumbali,+ ndipo mumtima mwawo anabwerera ku Iguputo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena