Ekisodo 16:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Ndipo ana a Isiraeli anali kunena kwa Mose ndi Aroni kuti: “Zikanakhala bwino dzanja la Yehova likanatiphera+ m’dziko la Iguputo, kumene tinali kudya nyama+ ndipo tinali kudya mkate ndi kukhuta. M’malomwake mwatibweretsa m’chipululu muno kuti muphetse mpingo wonsewu ndi njala.”+ Ekisodo 17:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Choncho anthu anamva ludzu pamenepo, ndipo anthuwo anapitiriza kung’ung’udzira Mose kuti: “N’chifukwa chiyani unatitulutsa mu Iguputo kuti udzatiphe ndi ludzu, ifeyo pamodzi ndi ana athu ndi ziweto zathu?”+ Numeri 14:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Ana onse a Isiraeli anayamba kudandaula za Mose ndi Aroni.+ Ndipo khamu lonselo linati: “Zikanakhala bwino tikanangofera ku Iguputo, kapena tikanangofera m’chipululu muno. Salimo 106:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Makolo athu ku Iguputo,Sanasonyeze kuzindikira kulikonse ntchito zanu zodabwitsa.+Sanakumbukire kuchuluka kwa kukoma mtima kwanu kosatha,+Koma anapanduka panyanja, pafupi ndi Nyanja Yofiira.+
3 Ndipo ana a Isiraeli anali kunena kwa Mose ndi Aroni kuti: “Zikanakhala bwino dzanja la Yehova likanatiphera+ m’dziko la Iguputo, kumene tinali kudya nyama+ ndipo tinali kudya mkate ndi kukhuta. M’malomwake mwatibweretsa m’chipululu muno kuti muphetse mpingo wonsewu ndi njala.”+
3 Choncho anthu anamva ludzu pamenepo, ndipo anthuwo anapitiriza kung’ung’udzira Mose kuti: “N’chifukwa chiyani unatitulutsa mu Iguputo kuti udzatiphe ndi ludzu, ifeyo pamodzi ndi ana athu ndi ziweto zathu?”+
2 Ana onse a Isiraeli anayamba kudandaula za Mose ndi Aroni.+ Ndipo khamu lonselo linati: “Zikanakhala bwino tikanangofera ku Iguputo, kapena tikanangofera m’chipululu muno.
7 Makolo athu ku Iguputo,Sanasonyeze kuzindikira kulikonse ntchito zanu zodabwitsa.+Sanakumbukire kuchuluka kwa kukoma mtima kwanu kosatha,+Koma anapanduka panyanja, pafupi ndi Nyanja Yofiira.+