Ekisodo 30:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Guwalo uliike kutsogolo kwa nsalu yotchinga imene ili pafupi ndi likasa la umboni.+ Likhale patsogolo pa chivundikiro chimene chili pamwamba pa Umboni,* pomwe ndidzaonekera kwa iwe.+ Levitiko 16:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Pamenepo Yehova anauza Mose kuti: “Uza Aroni m’bale wako, kuti asamalowe konse m’malo oyera+ kuseri kwa nsalu yotchinga,+ patsogolo pa chivundikiro cha Likasa, kuopera kuti angafe,+ chifukwa ine ndidzaonekera mu mtambo+ pamwamba pa chivundikirocho.+ Numeri 7:89 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 89 Nthawi zonse Mose akalowa m’chihema chokumanako kukalankhula ndi Mulungu,+ anali kumva mawu kuchokera pamwamba pa likasa la umboni akulankhula naye. Mawuwo anali kuchokera pachivundikiro+ chimene chinali palikasa la umboni, pakati pa akerubi awiri.+ Mulungu anali kulankhula naye motero. Oweruza 20:27 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 27 Kenako ana a Isiraeli anafunsira kwa Yehova,+ chifukwa masiku amenewo likasa la pangano+ la Mulungu woona linali ku Beteli komweko. Salimo 80:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 80 Inu M’busa wa Isiraeli, tcherani khutu,+Inu amene mukutsogolera Yosefe ngati gulu la nkhosa.+Inu amene mwakhala pa akerubi,+ walani.+
6 Guwalo uliike kutsogolo kwa nsalu yotchinga imene ili pafupi ndi likasa la umboni.+ Likhale patsogolo pa chivundikiro chimene chili pamwamba pa Umboni,* pomwe ndidzaonekera kwa iwe.+
2 Pamenepo Yehova anauza Mose kuti: “Uza Aroni m’bale wako, kuti asamalowe konse m’malo oyera+ kuseri kwa nsalu yotchinga,+ patsogolo pa chivundikiro cha Likasa, kuopera kuti angafe,+ chifukwa ine ndidzaonekera mu mtambo+ pamwamba pa chivundikirocho.+
89 Nthawi zonse Mose akalowa m’chihema chokumanako kukalankhula ndi Mulungu,+ anali kumva mawu kuchokera pamwamba pa likasa la umboni akulankhula naye. Mawuwo anali kuchokera pachivundikiro+ chimene chinali palikasa la umboni, pakati pa akerubi awiri.+ Mulungu anali kulankhula naye motero.
27 Kenako ana a Isiraeli anafunsira kwa Yehova,+ chifukwa masiku amenewo likasa la pangano+ la Mulungu woona linali ku Beteli komweko.
80 Inu M’busa wa Isiraeli, tcherani khutu,+Inu amene mukutsogolera Yosefe ngati gulu la nkhosa.+Inu amene mwakhala pa akerubi,+ walani.+