-
Levitiko 24:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Aroni azikhazika nyale pamalo ake, kunja kwa nsalu yotchinga ya Umboni m’chihema chokumanako. Nyaleyo iziunikira pamaso pa Yehova nthawi zonse kuyambira madzulo mpaka m’mawa. Limeneli ndi lamulo kwa inu mpaka kalekale m’mibadwo yanu yonse.
-
-
2 Mbiri 13:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Iwo akufukiza nsembe zopsereza kwa Yehova m’mawa uliwonse ndi madzulo alionse.+ Akufukizanso mafuta onunkhira+ ndipo mikate yosanjikiza ili patebulo la golide woyenga bwino.+ Tilinso ndi choikapo nyale chagolide+ ndi nyale zake zimene amayatsa madzulo alionse.+ Tikuchita zimenezi chifukwa tikukwaniritsa udindo wathu+ kwa Yehova Mulungu wathu, koma inuyo mwamusiya.+
-