Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 5:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 “‘Koma ngati sangakwanitse+ kupereka njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda, azibweretsa ufa wosalala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa.*+ Azibweretsa ufa umenewu monga nsembe yake chifukwa cha tchimo limene anachitalo, kuti ukhale nsembe yamachimo. Asauthire mafuta+ ndipo asaikemo lubani, chifukwa imeneyi ndi nsembe yamachimo.+

  • Nehemiya 13:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Eliyasibu anakonzera Tobia chipinda chachikulu chodyeramo+ m’chipinda chimene nthawi zonse anali kuikamo nsembe yambewu,+ lubani,* ziwiya, chakhumi cha mbewu, vinyo watsopano+ ndi mafuta+ zimene Alevi,+ oimba ndi alonda a pazipata anayenera kulandira, komanso zimene anali kupereka kwa ansembe.

  • Nyimbo ya Solomo 3:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 “Kodi chinthu chikuchokera kuchipululuchi n’chiyani, chooneka ngati utsi wokwera m’mwamba, chonunkhira mafuta a mule, lubani,*+ ndi mtundu uliwonse wa zonunkhira za ufa za munthu wamalonda?”+

  • Mateyu 2:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Tsopano atalowa m’nyumbamo, anaona mwanayo ndi mayi ake Mariya. Choncho anagwada ndi kumuweramira. Kenako anamasula chuma chawo ndi kupereka kwa mwanayo mphatso za golide, lubani ndi mule.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena