Nyimbo ya Solomo
3 “Pabedi panga usiku, ndinaganizira za munthu amene mtima wanga umam’konda.+ Ndinalakalaka kumuona koma iye panalibe. 2 Chotero ndinati: ‘Ndidzuke ndikazungulire mumzinda,+ m’misewu ndi m’mabwalo a mumzinda,+ kuti ndikafunefune munthu amene mtima wanga umam’konda.’ Ndinam’funafuna koma sindinamupeze. 3 Alonda+ amene anali kuzungulira mumzindawo anandipeza, ndipo ine ndinawafunsa kuti: ‘Kodi amuna inu, mwamuonako munthu amene mtima wanga umam’konda?’ 4 Nditangowapitirira pang’ono, ndinam’peza munthu amene mtima wanga umam’konda. Ndinamugwira ndipo sindinafune kum’siya mpaka nditamubweretsa m’nyumba mwa mayi anga, m’chipinda chamkati cha mayi amene anali ndi pakati kuti ine ndibadwe. 5 Ndakulumbiritsani inu+ ana aakazi a ku Yerusalemu, pali mbawala zazikazi ndiponso pali mphoyo zakutchire,+ kuti musayese kudzutsa chikondi mwa ine mpaka pamene chikondicho chifunire.”+
6 “Kodi chinthu chikuchokera kuchipululuchi n’chiyani, chooneka ngati utsi wokwera m’mwamba, chonunkhira mafuta a mule, lubani,*+ ndi mtundu uliwonse wa zonunkhira za ufa za munthu wamalonda?”+
7 “Taonani! Ndi bedi la Solomo. Amuna 60 amphamvu ochokera mwa amuna amphamvu a Isiraeli alizungulira.+ 8 Onsewo atenga malupanga ndipo ndi ophunzitsidwa nkhondo. Aliyense wamangirira lupanga lake m’chiuno mwake kuti adziteteze ku zoopsa za usiku.”+
9 “Ndi bedi* limene Mfumu Solomo inadzipangira ndi mitengo ya ku Lebanoni.+ 10 Mizati yake ndi yasiliva. Motsamira mwake ndi mwagolide. Pokhalira pake ndi popangidwa ndi ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira. Mkati mwake, ana aakazi a ku Yerusalemu akongoletsamo posonyeza chikondi.”
11 “Inu ana aakazi a Ziyoni, pitani panja mukaone Mfumu Solomo itavala nkhata yamaluwa,+ imene mayi ake+ anailukira pa tsiku la ukwati wake, pa tsiku limene mtima wa mfumuyo unasangalala.”+