3Tsopano Mose anakhala m’busa wa ziweto za Yetero,*+ wansembe wa ku Midiyani, amene anali apongozi ake.+ Pamene anali kuweta ziwetozo chakumadzulo kwa chipululu, anafika kuphiri la Mulungu woona,+ ku Horebe.+
16 Ulemerero wa Yehova+ unakhalabe paphiri la Sinai,+ ndipo mtambowo unakutabe phirilo kwa masiku 6. Ndiyeno pa tsiku la 7, Mulungu anaitana Mose kuchokera mumtambowo.+