17 Chipilala chilichonse kutalika kwake chinali mikono 18,+ ndipo mutu+ wake unali wamkuwa. Mutuwo kutalika kwake kunali mikono itatu, ndipo maukonde ndi makangaza+ amene anazungulira mutuwo, onse anali amkuwa. Chipilala chachiwiri chinalinso ndi maukonde ofanana ndi amenewa.