9 Ndiyeno Aroni ndi ana akewo uwamange malamba a pamimba. Ana akewo uwakulunge mipango kumutu kwawo ndipo unsembe udzakhala wawo. Limeneli ndi lamulo langa mpaka kalekale.+ Choncho upatse Aroni ndi ana ake mphamvu. +
13 Kenako Mose anaitana ana a Aroni+ ndi kuwaveka mikanjo, kuwamanga malamba a pamimba,+ ndi kuwakulunga mipango+ kumutu, monga mmene Yehova analamulira Mose.