4 Komabe Farao sadzakumverani,+ motero ndidzaonetsa mphamvu ya dzanja langa pa Iguputo ndi kutulutsa makamu anga,+ anthu anga,+ ana a Isiraeli,+ m’dziko la Iguputo ndi ziweruzo zamphamvu.+
35 Mose ameneyo, amene iwo anamukana ndi kunena kuti, ‘Iweyo anakuika ndani kuti ukhale wolamulira ndi woweruza wathu?’+ munthu ameneyo ndi amene Mulungu anamutumiza+ monga wolamulira ndi mpulumutsi kudzera mwa mngelo amene anaonekera kwa iye pachitsamba chaminga chija.