Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Genesis 41:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Kutacha m’mawa, Farao anavutika kwambiri ndi maganizo.+ Chotero anaitanitsa ansembe onse amatsenga+ ndi amuna anzeru+ onse a mu Iguputo, n’kuwafotokozera maloto akewo.+ Koma palibe amene anatha kum’masulira Farao malotowo.

  • Yesaya 19:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Akalonga a ku Zowani+ ndi opusa ndithu. Malangizo a anthu anzeru ochokera pakati pa alangizi a Farao, ndi osathandiza.+ Kodi anthu inu mudzamuuza bwanji Farao kuti: “Ine ndine mwana wa anthu anzeru, mwana wa mafumu akale”?

  • Yeremiya 27:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 “‘“‘Anthu inu musamvere aneneri,+ ochita zamaula, olota maloto,+ ochita zamatsenga ndi obwebweta+ amene ali pakati panu ndipo akukuuzani kuti: “Anthu inu simudzatumikira mfumu ya Babulo.”+

  • Danieli 2:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Pamenepo mfumuyo inalamula kuti aitane ansembe onse ochita zamatsenga,+ anthu olankhula ndi mizimu, Akasidi* ndi anthu ena ochita zamatsenga kuti adzauze mfumu maloto akewo.+ Anthu amenewa anafika ndi kuima pamaso pa mfumu.

  • 2 Timoteyo 3:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Tsopano monga mmene Yane ndi Yambure+ anatsutsira Mose, anthu amenewanso akupitiriza kutsutsa choonadi.+ Iwo ali ndi maganizo opotoka kwambiri,+ ndipo sakuyenerera chikhulupirirochi.+

  • Chivumbulutso 21:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Koma amantha, opanda chikhulupiriro,+ odetsedwa amenenso amachita zinthu zonyansa,+ opha anthu,+ adama,+ ochita zamizimu, opembedza mafano,+ ndi onse abodza,+ gawo lawo lidzakhala m’nyanja yoyaka moto+ ndi sulufule.+ Nyanja imeneyi ikuimira imfa yachiwiri.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena