-
Yesaya 30:17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Anthu 1,000 adzanjenjemera chifukwa cha mawu oopseza a munthu mmodzi.+ Ndipo chifukwa cha mawu oopseza a anthu asanu, inuyo mudzathawa mpaka mudzatsala ochepa ngati mtengo wautali wa pangalawa wozikidwa pamwamba pa phiri, ndiponso ngati mtengo wozikidwa pamwamba pa phiri laling’ono kuti ukhale chizindikiro.+
-
-
Ezekieli 21:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Ndiyeno akakufunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani ukubuula?’+ Uwayankhe kuti, ‘N’chifukwa cha uthenga umene ndamva.’+ Pakuti uthengawo udzafika ndithu+ ndipo mtima wa munthu aliyense udzasungunuka ndi mantha.+ Anthu onse adzazizira nkhongono. Aliyense adzataya mtima ndipo mawondo onse adzachucha madzi.*+ ‘Uthengawo ufika ndithu+ ndipo zimene ukunena zidzachitikadi,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”
-