Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 28:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Yehova adzakuchititsani kuti mugonje pamaso pa adani anu.+ Pokamenyana nawo nkhondo mudzadutsa njira imodzi, koma pothawa pamaso pawo mudzadutsa njira 7. Mudzakhala chinthu chonyansa kwa mafumu onse a dziko lapansi.+

  • Oweruza 2:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakira Isiraeli,+ moti anawapereka m’manja mwa ofunkha, ndipo anayamba kufunkha zinthu zawo.+ Iye anawagulitsa kwa adani awo owazungulira+ moti sanathe kuima pamaso pa adani awo.+

  • 1 Samueli 4:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Chotero Afilisiti anamenyadi nkhondo, ndipo Aisiraeli anagonja+ moti aliyense wa iwo anayamba kuthawira kuhema wake.+ Ndipo amene anaphedwa anali ochuluka kwambiri.+ Panaphedwa amuna oyenda pansi a Isiraeli okwanira 30,000.+

  • Maliro 2:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Yehova wachita zimene anali kuganiza.+ Wakwaniritsa zimene ananena,+

      Zimene analamula kalekale.+ Wapasula zinthu ndipo sanamve chisoni.+

      Wachititsa adani ako kusangalala+ chifukwa cha zimene zakuchitikira. Wakweza nyanga ya adani+ ako.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena