15 Munthu aliyense amene wadya nyama imene waipeza yakufa, kapena yophedwa ndi chilombo,+ kaya akhale nzika kapena mlendo wokhala pakati panu, munthu ameneyo azichapa zovala zake ndi kusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa kufikira madzulo.+ Kenako azikhala woyera.