Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 20:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Mwamuna akakwatira mkazi wa m’bale wake, wachita chinthu chonyansa.+ Iye wavula m’bale wake. Mwamuna ndi mkaziyo ayenera kufa kuti asabereke ana.

  • Deuteronomo 25:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 “Ngati amuna apachibale akukhala moyandikana, ndiyeno mmodzi n’kumwalira asanabereke mwana wamwamuna, mkazi wa womwalirayo asakwatiwe ndi mlendo wochokera m’banja lina. Mlamu wake apite kwa iye ndi kum’tenga kukhala mkazi wake, ndipo achite ukwati wa pachilamu.+

  • Maliko 6:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Pakuti Herodeyo anatumiza anthu kukagwira Yohane, kum’manga ndi kum’tsekera m’ndende, chifukwa Herode anakwatira Herodiya, mkazi wa m’bale wake Filipo.+

  • Maliko 12:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 “Mphunzitsi, Mose anatilembera kuti ngati munthu wamwalira ndi kusiya mkazi koma osasiya mwana, m’bale wake+ atenge mkazi wamasiyeyo ndi kuberekera m’bale wake uja ana mwa mkaziyo.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena