Ekisodo 20:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 “Usadzipangire fano kapena chifaniziro cha chinthu chilichonse chakumwamba, kapena chapadziko lapansi, kapenanso cham’madzi a padziko lapansi.*+ Levitiko 26:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 “‘Musadzipangire milungu yopanda pake,+ chifaniziro,+ kapena chipilala chopatulika. Musaike mwala wokhala ndi zithunzi zojambula mochita kugoba+ m’dziko lanu kuti muziugwadira,+ chifukwa ine ndine Yehova Mulungu wanu. Salimo 96:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Chifukwa milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi milungu yopanda pake,+Koma Yehova ndiye anapanga kumwamba.+ Habakuku 2:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Kodi chifaniziro chosema, chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula ndiponso mphunzitsi wonama,+ zili ndi phindu lanji+ kuti wozipanga azizikhulupirira+ ndipo azipanga milungu yopanda pake yosalankhula?+ 1 Akorinto 10:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Ndiye chifukwa chake, okondedwa anga, thawani+ kupembedza mafano.+
4 “Usadzipangire fano kapena chifaniziro cha chinthu chilichonse chakumwamba, kapena chapadziko lapansi, kapenanso cham’madzi a padziko lapansi.*+
26 “‘Musadzipangire milungu yopanda pake,+ chifaniziro,+ kapena chipilala chopatulika. Musaike mwala wokhala ndi zithunzi zojambula mochita kugoba+ m’dziko lanu kuti muziugwadira,+ chifukwa ine ndine Yehova Mulungu wanu.
5 Chifukwa milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi milungu yopanda pake,+Koma Yehova ndiye anapanga kumwamba.+
18 Kodi chifaniziro chosema, chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula ndiponso mphunzitsi wonama,+ zili ndi phindu lanji+ kuti wozipanga azizikhulupirira+ ndipo azipanga milungu yopanda pake yosalankhula?+