18 Koma ngati nyama iliyonse ya nsembe yachiyanjano yadyedwa pa tsiku lachitatu, wopereka nsembeyo sadzayanjidwa ndi Mulungu.+ Nsembe yakeyo sadzapindula nayo.+ Idzakhala chinthu chonyansa, ndipo amene wadyako nsembeyo adzadziyankhira mlandu wa cholakwa chake.+