5 Inu anthu anga, chonde kumbukirani+ zimene Balaki mfumu ya Mowabu anakonza kuti achite+ ndiponso zimene Balamu mwana wa Beori anamuyankha.+ Kumbukirani zimene zinachitika kuyambira ku Sitimu+ kukafika ku Giligala.+ Zimenezo zinachitika n’cholinga chakuti zochita za Yehova zolungama zidziwike.”+