24 “Aroni aikidwe m’manda, agone ndi makolo ake,+ pakuti sadzalowa m’dziko limene ndidzapatse ana a Isiraeli. Izi zili choncho chifukwa amuna inu munapandukira malangizo anga okhudza madzi a ku Meriba.+
38 Wansembe Aroni anakwera m’phiri la Hora monga mmene Yehova anamulamulira, ndipo anamwalira ali m’phirimo. Anamwalira m’chaka cha 40 kuchokera pamene ana a Isiraeli anatuluka m’dziko la Iguputo, m’mwezi wachisanu, pa tsiku loyamba la mweziwo.+
6 “Pamenepo ana a Isiraeli ananyamuka kuchoka ku Beeroti Bene-yaakana+ kupita ku Mosera. Aroni anafera kumalo amenewo, ndipo anamuikanso kumeneko.+ Mwana wake Eleazara anayamba kutumikira monga wansembe m’malo mwa Aroniyo.+
50 Pamenepo ukafera m’phiri limene ukukwera ndi kugona ndi makolo ako,+ monga mmene Aroni m’bale wako anafera m’phiri la Hora+ ndi kugona ndi makolo ake.