-
Numeri 15:24Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 ngati khamulo lachita cholakwacho mosazindikira, pamenepo khamu lonselo lipereke ng’ombe yaing’ono yamphongo monga nsembe yopsereza yafungo lokhazika mtima pansi kwa Yehova. Apereke nsembeyo limodzi ndi nsembe yake yambewu ndiponso nsembe yake yachakumwa monga mwa dongosolo la nthawi zonse.+ Aperekenso mwana wa mbuzi mmodzi monga nsembe yamachimo.+
-