Deuteronomo 23:21 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 21 “Ukapereka lonjezo kwa Yehova+ Mulungu wako usachedwe kulikwaniritsa kuopera kuti ungachimwe,+ chifukwa Yehova Mulungu wako adzafuna ndithu kuti ukwaniritse chimene walonjezacho.+ Salimo 76:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Inu nonse amene mwazungulira Mulungu, lonjezani ndi kukwaniritsa malonjezo anuwo kwa Yehova Mulungu wanu.+Bweretsani mphatso mwamantha.+ Salimo 116:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova,+Pamaso pa anthu ake onse. Salimo 119:106 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 106 Ndalumbira kuti ndidzasunga zigamulo zanu zolungama,+Ndipo ndidzakwaniritsa lumbiro langa.+ Mlaliki 5:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Ukalonjeza kwa Mulungu usamachedwe kukwaniritsa lonjezo lako,+ chifukwa palibe amene amasangalala ndi anthu opusa.+ Uzikwaniritsa zinthu zimene walonjeza.+ Mateyu 5:33 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 33 “Komanso munamva kuti anthu akale anauzidwa kuti, ‘Usamalumbire+ koma osachita, m’malomwake uzikwaniritsa malonjezo ako kwa Yehova.’+
21 “Ukapereka lonjezo kwa Yehova+ Mulungu wako usachedwe kulikwaniritsa kuopera kuti ungachimwe,+ chifukwa Yehova Mulungu wako adzafuna ndithu kuti ukwaniritse chimene walonjezacho.+
11 Inu nonse amene mwazungulira Mulungu, lonjezani ndi kukwaniritsa malonjezo anuwo kwa Yehova Mulungu wanu.+Bweretsani mphatso mwamantha.+
4 Ukalonjeza kwa Mulungu usamachedwe kukwaniritsa lonjezo lako,+ chifukwa palibe amene amasangalala ndi anthu opusa.+ Uzikwaniritsa zinthu zimene walonjeza.+
33 “Komanso munamva kuti anthu akale anauzidwa kuti, ‘Usamalumbire+ koma osachita, m’malomwake uzikwaniritsa malonjezo ako kwa Yehova.’+