24 Koma mtumiki wanga Kalebe,+ chifukwa wasonyeza kuti ali ndi mzimu wosiyana ndi wa ena, ndipo wakhala akunditsatira ndi mtima wonse,+ ndithudi ndidzam’lowetsa m’dziko limene anakalizonda, ndipo mbadwa zake zidzakhalamo ngati dziko lawo.+
36 kupatulapo Kalebe mwana wa Yefune.+ Iyeyu adzaliona, ndipo ndidzagawira dziko limene anafikako kwa iye ndi ana ake, chifukwa chakuti watsatira Yehova ndi mtima wonse.+