Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Numeri 14:33
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 33 Ana anu adzakhala abusa m’chipululu+ kwa zaka 40, ndipo adzavutika chifukwa cha kusakhulupirika*+ kwanu, mpaka womalizira kufa wa inu atagona m’manda m’chipululu.+

  • Deuteronomo 29:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 ‘Pamene ndinali kukutsogolerani kwa zaka 40 m’chipululu,+ zovala zanu sizinathe ndiponso nsapato zanu sizinathe kumapazi anu.+

  • Yoswa 5:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Ana a Isiraeliwo anayenda m’chipululu zaka 40,+ mpaka amuna onse otha kupita kunkhondo amene anatuluka mu Iguputo atatha, amene sanamvere mawu a Yehova. Amenewo Yehova anawalumbirira kuti sadzawalola kuona dziko+ limene Yehova analumbirira makolo awo kuti adzalipereka kwa anthu ake,*+ dziko loyenda mkaka ndi uchi.+

  • Salimo 95:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Kwa zaka 40, m’badwo umenewo unali kundinyansa,+

      Ndipo ndinati:

      “Anthu awa mitima yawo imasochera,+

      Ndipo sadziwa njira zanga.”+

  • Machitidwe 7:36
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 36 Munthu ameneyo anawatsogolera ndi kutuluka nawo,+ atachita zodabwitsa ndi zizindikiro mu Iguputo,+ pa Nyanja Yofiira+ ndi m’chipululu kwa zaka 40.+

  • Machitidwe 13:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Kwa nthawi ya zaka pafupifupi 40,+ anapirira khalidwe lawo m’chipululu.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena