3 Mukonze nsembeyo pa tsiku la 14 la mwezi uno, madzulo kuli kachisisira,*+ ndiyo nthawi yake yoikidwiratu. Muikonze malinga ndi malamulo ake onse, ndiponso motsatira njira zonse za kakonzedwe kake.”+
16“Muzisunga mwambo wa m’mwezi wa Abibu*+ pochita chikondwerero cha pasika kwa Yehova Mulungu wanu,+ chifukwa m’mwezi wa Abibu Yehova Mulungu wanu anakutulutsani mu Iguputo usiku.+