40 Choncho Yoswa anapha anthu a m’dera lonse la mapiri,+ anthu a ku Negebu,+ a ku Sefela,+ ndi a m’madera otsetsereka+ pamodzi ndi mafumu awo onse. Iye anaonetsetsa kuti pasakhale wopulumuka,+ ndipo anapha chamoyo chilichonse+ monga mmene Yehova Mulungu wa Isiraeli analamulira.+