12 Anatengera anthu ogwidwawo limodzi ndi zofunkha zina zonse kwa Mose, wansembe Eleazara, ndi kwa khamu la ana a Isiraeli. Anapita nawo kumsasa wawo ku Yeriko, pafupi ndi mtsinje wa Yorodano, m’chipululu cha Mowabu.+
13 Amenewa ndiwo malamulo+ ndi zigamulo za Yehova, zimene anapereka kwa ana a Isiraeli kudzera kwa Mose ku Yeriko, m’chipululu cha Mowabu, pafupi ndi mtsinje wa Yorodano.+