24 Amenewa ndiwo anali ana a Levi potsata nyumba ya makolo awo.+ Iwowa anali atsogoleri a nyumba ya makolo awo, ndipo mmodzi ndi mmodzi anapatsidwa udindo potsata mndandanda wa mayina awo. Amenewa anali oti azigwira ntchito yotumikira+ panyumba ya Yehova kuyambira azaka 20 kupita m’tsogolo.+
13 Anam’patsanso malangizo okhudza magulu+ a ansembe ndi a Alevi, ntchito yonse yokhudza utumiki wa panyumba ya Yehova, ndiponso malangizo okhudza ziwiya zonse za utumiki wa panyumba ya Yehova.