4 ndipo iyeyo analowa m’chipululu n’kuyenda ulendo wa tsiku limodzi. Kenako anafika pa kamtengo kenakake,+ ndipo anakhala pansi pake. Ndiyeno anayamba kupempha kuti afe, ponena kuti: “Basi ndatopa nazo. Tsopano chotsani moyo wanga+ Yehova, pakuti sindine woposa makolo anga.”