13 Ndipo azipha nkhosa yaing’ono yamphongoyo pamalo+ amene nthawi zonse amapherapo nyama ya nsembe yamachimo ndi nsembe yopsereza, pamalo oyera.+ Azichita zimenezi chifukwa nsembe ya kupalamula ndi ya wansembe+ mofanana ndi nsembe yamachimo. Nsembe ya kupalamula ndi yopatulika koposa.