20 Koma iye anakanabe, kuti: “Ayi, musadzere+ m’dziko langa.” Mfumu ya Edomu+ itanena zimenezi, inatuluka ndi chikhamu cha anthu, ndi gulu la asilikali lamphamvu, kuti akawathire nkhondo.
4 Pamene Aisiraeliwo anali pa ulendo kuchokera kuphiri la Hora+ kudzera njira yopita ku Nyanja Yofiira, kulambalala dziko la Edomu,+ anayamba kutopa chifukwa cha njirayo.
18 Pamene anali kudutsa m’chipululu, anayenda molambalala dziko la Edomu+ ndi dziko la Mowabu, moti anadutsa chakum’mawa kwa dziko la Mowabu+ ndi kukamanga misasa m’chigawo cha Arinoni. Iwo sanadutse malire a Mowabu,+ chifukwa Arinoni ndiye anali malire a Mowabu.+