13 Atasamuka kumeneko anakamanga msasa m’dera la chigwa cha Arinoni,+ m’chipululu chochokera kumalire a dziko la Aamori. Chigwa cha Arinoni chinali malire pakati pa dziko la Mowabu ndi la Aamori.
17 Kenako anatumiza mithenga kwa mfumu ya Edomu+ kuti: “Tiloleni tidutse m’dziko lanu,” koma mfumu ya Edomu sinamvere. Anatumizanso mithenga kwa mfumu ya Mowabu,+ koma nayonso sinavomereze. Choncho Aisiraeli anapitiriza kukhala ku Kadesi.+
10 Tsopano taonani zimene akuchita ana a Amoni,+ ana a Mowabu+ ndi a kudera lamapiri la Seiri.+ Inu simunalole kuti Aisiraeli alowe m’dziko lawo pamene anali kutuluka m’dziko la Iguputo ndipo anawasiya osawawononga.+