-
Ekisodo 32:27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 Pamenepo iye anawauza kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Aliyense wa inu amange lupanga lake m’chiuno mwake. Ndiyeno mudutse mkati mwa msasa ndi kuyenda mobwerezabwereza, kuchoka pachipata china kufika pachipata china, ndipo aliyense wa inu aphe m’bale wake, mnzake ndi mnzake wapamtima.’”+
-
-
Levitiko 10:6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Atatero Mose anauza Aroni ndi ana ake ena, Eleazara ndi Itamara, kuti: “Musalekerere tsitsi lanu osalisamala,+ ndipo musang’ambe zovala zanu kuti mungafe ndiponso kuti Mulungu angakwiyire khamu lonseli.+ Abale anu, nyumba yonse ya Isiraeli ndiwo alire chifukwa cha kuwononga ndi moto kumene Yehova wachita.
-