Deuteronomo 17:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Akakhala pampando wachifumu, ayenera kukopera buku lakelake la chilamulo ichi, kuchokera m’buku limene ansembe achilevi amasunga.+ Deuteronomo 27:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Ndiyeno mukawoloka,+ mulembe pamiyalapo mawu onse a chilamulochi+ kuti mulowe m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, dziko loyenda mkaka ndi uchi, malinga ndi zimene Yehova Mulungu wa makolo anu wakuuzani.+ Malaki 4:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 “Anthu inu kumbukirani chilamulo cha Mose mtumiki wanga. Kumbukirani malamulo ndi zigamulo zimene ndinam’patsa ku Horebe zokhudza Aisiraeli onse.+ Yohane 1:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Popeza Chilamulo chinaperekedwa kudzera mwa Mose,+ kukoma mtima kwakukulu+ komanso choonadi+ zinakhalako kudzera mwa Yesu Khristu. Agalatiya 3:24 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 24 N’chifukwa chake Chilamulo chakhala mtsogoleri* wotifikitsa kwa Khristu,+ kuti tiyesedwe olungama+ chifukwa cha chikhulupiriro.
18 Akakhala pampando wachifumu, ayenera kukopera buku lakelake la chilamulo ichi, kuchokera m’buku limene ansembe achilevi amasunga.+
3 Ndiyeno mukawoloka,+ mulembe pamiyalapo mawu onse a chilamulochi+ kuti mulowe m’dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, dziko loyenda mkaka ndi uchi, malinga ndi zimene Yehova Mulungu wa makolo anu wakuuzani.+
4 “Anthu inu kumbukirani chilamulo cha Mose mtumiki wanga. Kumbukirani malamulo ndi zigamulo zimene ndinam’patsa ku Horebe zokhudza Aisiraeli onse.+
17 Popeza Chilamulo chinaperekedwa kudzera mwa Mose,+ kukoma mtima kwakukulu+ komanso choonadi+ zinakhalako kudzera mwa Yesu Khristu.
24 N’chifukwa chake Chilamulo chakhala mtsogoleri* wotifikitsa kwa Khristu,+ kuti tiyesedwe olungama+ chifukwa cha chikhulupiriro.