Genesis 15:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Kenako anamutengera panja, n’kumuuza kuti: “Kweza maso ako kumwamba, uwerenge nyenyezizo ngati ungathe kuziwerenga.”+ Ndipo anamuuzanso kuti: “Umu ndi mmene mbewu yako idzakhalire.”+ Deuteronomo 1:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Yehova Mulungu wanu wakuchulukitsani ndipo onani lero mwachulukadi ngati nyenyezi zakuthambo.+ Nehemiya 9:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Ndipo munawachulukitsira ana awo ngati nyenyezi zakumwamba.+ Mutatero munawalowetsa m’dziko+ limene munalonjeza makolo awo+ kuti akalowe ndi kulitenga.
5 Kenako anamutengera panja, n’kumuuza kuti: “Kweza maso ako kumwamba, uwerenge nyenyezizo ngati ungathe kuziwerenga.”+ Ndipo anamuuzanso kuti: “Umu ndi mmene mbewu yako idzakhalire.”+
23 Ndipo munawachulukitsira ana awo ngati nyenyezi zakumwamba.+ Mutatero munawalowetsa m’dziko+ limene munalonjeza makolo awo+ kuti akalowe ndi kulitenga.